Aefeso 5:25, 26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu+ ngati mmenenso Khristu anakondera mpingo nʼkudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo,+ 26 nʼcholinga choti auyeretse pousambitsa mʼmadzi a mawu a Mulungu.+ 1 Atesalonika 5:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Mulungu wamtendereyo akupatuleni kuti muchite utumiki wake. Ndipo pa mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu komanso thupi lanu, zikhale zopanda chilema kapena cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 2 Atesalonika 2:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Komabe, tiyenera kumathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale amene Yehova* amakukondani, chifukwa Mulungu anakusankhani kuchokera pachiyambi+ kuti mudzapulumuke. Anachita zimenezi pokuyeretsani+ ndi mzimu wake komanso chifukwa munakhulupirira choonadi. 1 Petulo 1:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+
25 Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu+ ngati mmenenso Khristu anakondera mpingo nʼkudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo,+ 26 nʼcholinga choti auyeretse pousambitsa mʼmadzi a mawu a Mulungu.+
23 Mulungu wamtendereyo akupatuleni kuti muchite utumiki wake. Ndipo pa mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu komanso thupi lanu, zikhale zopanda chilema kapena cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+
13 Komabe, tiyenera kumathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale amene Yehova* amakukondani, chifukwa Mulungu anakusankhani kuchokera pachiyambi+ kuti mudzapulumuke. Anachita zimenezi pokuyeretsani+ ndi mzimu wake komanso chifukwa munakhulupirira choonadi.
22 Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+