20 Ndiyeno mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12+ anafika kumbuyo kwake nʼkugwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ 21 chifukwa mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”