-
Genesis 37:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Tsiku linanso analota maloto ena, ndipo anauza abale akewo kuti: “Leronso ndinalota maloto ena. Ndinalota dzuwa ndi mwezi ndiponso nyenyezi zokwana 11 zikundigwadira.”+ 10 Kenako anafotokozeranso bambo ake ndi abale ake malotowo. Koma bambo ake anamʼdzudzula kuti: “Kodi maloto akowa akutanthauza chiyani? Kodi zoona ineyo ndi mayi akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?” 11 Abale akewo anamuchitira nsanje,+ koma bambo ake anasunga mawuwo mumtima.
-