Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 2:11-15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Tsopano mʼmasiku amenewo, Mose atakula* anapita kwa abale ake kuti akaone mmene ankavutikira ndi ntchito yaukapolo+ imene ankagwira. Kumeneko anaona mʼbale wake wa Chiheberi akumenyedwa ndi nzika ina ya ku Iguputo. 12 Choncho anayangʼana uku ndi uku ndipo ataona kuti palibe amene akumuona, anapha munthu wa ku Iguputoyo nʼkumubisa mumchenga.+

      13 Koma tsiku lotsatira atapitanso, anapeza amuna awiri a Chiheberi akumenyana. Choncho anafunsa wolakwayo kuti: “Ukumʼmenyeranji mnzako?”+ 14 Poyankha iye anati: “Ndi ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza? Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera nzika ya mu Iguputo ija?”+ Zitatero Mose anachita mantha ndipo mumtima mwake anati: “Apa nkhani ija yadziwika basi!”

      15 Kenako Farao anamva za nkhaniyi ndipo ankafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa Farao nʼkupita kukakhala kudziko la Midiyani.+ Atafika kumeneko, anakhala pafupi ndi chitsime.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena