25 Inu amʼnyumba ya Isiraeli,
Kodi pamene munali mʼchipululu muja kwa zaka 40, munandipatsa nsembe zanyama ndi zopereka zina?+
26 Koma inu mudzanyamula Sakuti mfumu yanu ndi Kaiwani,
Mafano amene munapanga a mulungu wanu wa nyenyezi.
27 Ndipo ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kwambiri ndi ku Damasiko,’+ watero Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, amene dzina lake ndi Yehova.”+