-
Machitidwe 17:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Pamapeto pake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira ndipo anagwirizana ndi Paulo ndi Sila.+ Agiriki ambiri opembedza Mulungu komanso azimayi ambiri olemekezeka anachitanso chimodzimodzi.
5 Koma Ayuda anachita nsanje+ ndipo anasonkhanitsa anthu ena oipa amene ankangokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa nʼkuyambitsa chipolowe mumzindamo. Kenako anapita kunyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse nʼkuwapereka ku gulu limene linkachita chipolowelo.
-