-
Aheberi 2:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 ndiye tidzapulumuka bwanji ngati titanyalanyaza chipulumutso chachikulu chonchi?+ Ambuye wathu ndi amene anayamba kunena za chipulumutsochi+ ndipo anthu amene anamumva anatitsimikizira zimenezo. 4 Mulungu nayenso anachitira umboni za chipulumutsochi pogwiritsa ntchito zizindikiro, zinthu zodabwitsa, ntchito zamphamvu zosiyanasiyana+ komanso mzimu woyera umene anaupereka mogwirizana ndi chifuniro chake.+
-