48 Ngati mlendo amene akukhala nanu akufuna kuchita nawo chikondwerero cha Pasika kwa Yehova, mwamuna aliyense wamʼnyumba yake adulidwe. Akatero angathe kubwera kudzachita nawo chikondwererocho, ndipo ayenera kuonedwa ngati mbadwa ya dzikolo. Koma munthu wosadulidwa asadye nawo.+