-
1 Yohane 2:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto. Munamva kuti wokana Khristu akubwera,+ ndipo panopa okana Khristu ambiri aonekera.+ Chifukwa cha zimenezi tikudziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto. 19 Amenewo anachoka pakati pathu, koma sanali mʼgulu lathu,*+ chifukwa akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe ndi ife. Koma anachoka kuti zidziwike kuti si onse amene ali mʼgulu lathu.+
-