-
1 Samueli 12:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ine ndaima pano. Mupereke umboni pamaso pa Yehova ndi pamaso pa wodzozedwa wake:+ Kodi alipo amene ndinamʼtengera ngʼombe kapena bulu wake?+ Nanga alipo amene ndinamʼchitirapo zachinyengo kapena kumʼpondereza? Kodi ndinalandirapo chiphuphu kwa aliyense kuti ndisachite chilungamo?+ Ngati ndinachitapo zimenezi, ndine wokonzeka kukubwezerani.”+
-
-
1 Akorinto 9:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ngati tinakupatsani zinthu zauzimu,* kodi nʼkulakwa kulandira* zinthu zofunika pa moyo kuchokera kwa inu?+ 12 Ngati anthu ena amayembekezera kuti muwachitire zimenezi, ndiye kuli bwanji ifeyo? Komatu ife sitinagwiritse ntchito ufulu umenewo.+ Koma timapirira zinthu zonse kuti tisalepheretse ena kumva uthenga wabwino wonena za Khristu.+
-