-
Aefeso 2:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Kuwonjezera pamenepo, Mulungu anapangitsa kuti mukhale amoyo ngakhale kuti munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu komanso machimo anu.+ 2 Pa nthawi ina munkachita zimenezi mogwirizana ndi nthawi* za mʼdzikoli,+ pomvera wolamulira wa mpweya+ umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe+ kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana osamvera.
-