-
Machitidwe 14:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ku Lusitara, kunali munthu wina wolumala miyendo ndipo anali atakhala pansi. Iyeyu anabadwa wolumala ndipo anali asanayendepo. 9 Munthu ameneyu ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Ndiyeno Paulo atamuyangʼanitsitsa anaona kuti ali ndi chikhulupiriro choti angachiritsidwe.+ 10 Choncho Paulo analankhula mokweza mawu kuti: “Imirira!” Atatero, wolumalayo anadumpha nʼkuyamba kuyenda.+
-