-
Afilipi 1:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndiye kodi zotsatira zake nʼzotani? Ndi zoti uthenga wokhudza Khristu ukufalitsidwabe, kaya ndi mwachiphamaso kapena mʼchoonadi ndipo ine ndikusangalala chifukwa cha zimenezi. Ndipotu ndipitirizabe kusangalala 19 chifukwa ndikudziwa kuti zimenezi zidzachititsa kuti ndipulumutsidwe chifukwa cha mapembedzero anu+ komanso ndi thandizo la mzimu wa Yesu Khristu.+ 20 Zimenezi nʼzogwirizana ndi zimene ndikudikirira mwachidwi ndiponso chiyembekezo changa chakuti sindidzachititsidwa manyazi mwa njira iliyonse. Koma kuti mwa ufulu wanga wonse wa kulankhula, tsopano Khristu alemekezedwa kudzera mwa ine,* ngati mmene zakhala zikuchitikira mʼmbuyo monsemu. Iye alemekezedwabe kaya ndikhala ndi moyo kapena ndimwalira.+
-