23 Ndipo mupitirize kusintha kuti mukhale atsopano pa kaganizidwe kanu komanso mmene mumaonera zinthu.+ 24 Ndipo muvale umunthu watsopano+ umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mukachita zimenezi mudzatha kuchita zimene zilidi zolungama ndi zokhulupirika.