Agalatiya 2:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Koma ataona kuti ndapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu osadulidwa,+ mofanana ndi Petulo amene anapatsidwa ntchito yoti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu odulidwa, Aefeso 3:1, 2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Choncho, ine Paulo, ndili mʼndende+ chifukwa ndili kumbali ya Khristu Yesu komanso chifukwa chothandiza inu, anthu a mitundu ina— 2 ndithudi, munamva kuti ndinalandira udindo wokuthandizani+ kuti mupindule ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, Akolose 1:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Ndinakhala mtumiki wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule.
7 Koma ataona kuti ndapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu osadulidwa,+ mofanana ndi Petulo amene anapatsidwa ntchito yoti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu odulidwa,
3 Choncho, ine Paulo, ndili mʼndende+ chifukwa ndili kumbali ya Khristu Yesu komanso chifukwa chothandiza inu, anthu a mitundu ina— 2 ndithudi, munamva kuti ndinalandira udindo wokuthandizani+ kuti mupindule ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,
25 Ndinakhala mtumiki wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule.