14 Ineyo sindikufuna kudzitama pa chifukwa china chilichonse, kupatulapo chifukwa cha mtengo wozunzikirapo wa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ Kwa ine, dziko linaweruzidwa kuti liphedwe kudzera mwa iye, koma malinga nʼkuona kwa dzikoli, ineyo ndinaweruzidwa kuti ndiphedwe kudzera mwa iye.