19 Koma ine, ndikuyembekeza kuti Ambuye Yesu andilola kutumiza Timoteyo+ kwa inu posachedwapa kuti ndidzalimbikitsidwe ndikadzamva mmene zinthu zilili kwa inu. 20 Chifukwa ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati wake, amene angasamaliredi moona mtima zosowa zanu.