-
Afilipi 3:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Chifukwa pali anthu ambiri amene akuchita zinthu ngati adani a mtengo wozunzikirapo* wa Khristu. Kale ndinkawatchula pafupipafupi koma pano ndimawatchula ndikugwetsa misozi. 19 Anthu amenewo akuyembekezera kuwonongedwa ndipo mulungu wawo ndi mimba zawo. Iwo amanyadira zinthu zimene akuyenera kuchita nazo manyazi ndipo amangoganizira zinthu zapadziko lapansi.+
-