Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Maliko 7:21, 22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Chifukwa mumtima mwa anthu+ mumatuluka maganizo oipa ngati: zachiwerewere,* zakuba, zopha anthu, 22 zachigololo, dyera, kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lopanda manyazi,* diso la kaduka, mawu onyoza, kudzikweza ndiponso kuchita zinthu mopanda nzeru.

  • Aefeso 4:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Popeza iwo sakuthanso kuzindikira makhalidwe abwino, anadzipereka okha ku khalidwe lopanda manyazi*+ kuti achite zonyansa zamtundu uliwonse mwadyera.

  • 2 Petulo 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kuwonjezera pamenepo, ambiri adzatengera khalidwe lopanda manyazi*+ la aphunzitsi abodzawo ndipo anthu azidzalankhula monyoza njira ya choonadi chifukwa cha aphunzitsiwo.+

  • Yuda 4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndatero chifukwa chakuti anthu ena alowa mozemba pakati panu. Malemba anasonyezeratu kalekale kuti anthu amenewa adzaweruzidwa. Anthuwa ndi osaopa Mulungu ndipo atenga kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lopanda manyazi.*+ Komanso asonyeza kuti ndi osakhulupirika kwa Ambuye wathu mmodzi yekha amene anatigula, Yesu Khristu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena