8 Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru+ chifukwa mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.+ 9 Choncho mukhale ndi chikhulupiriro cholimba ndipo mulimbane naye,+ podziwa kuti abale anu padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.+