-
2 Akorinto 11:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ndinalandira chithandizo kuchokera kumipingo ina ndipo zinali ngati ndikuwabera nʼcholinga choti nditumikire inuyo.+ 9 Koma pamene ndinasowa zofunika zina ndili kwanuko, sindinalemetse munthu aliyense, popeza abale amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkafunikira.+ Ndithu, ndinayesetsa kuti ndisakulemetseni mʼnjira iliyonse, ndipo ndipitirizabe kutero.+
-