-
2 Timoteyo 2:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Koma uzipewa nkhani zopeka zimene zimaipitsa zinthu zoyera+ chifukwa zimachititsa kuti anthu ambiri asamaope Mulungu, 17 ndipo mawu awo amafalikira ngati chilonda chonyeka. Ena mwa anthu amenewo ndi Hemenayo ndi Fileto.+ 18 Anthu amenewa akupotoza choonadi, ponena kuti akufa anauka kale+ ndipo akuwononga chikhulupiriro cha ena.
-