-
Ekisodo 20:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndiyeno anthu onse ankamva mabingu ndi kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, ankaona kungʼanima kwa mphezi ndiponso phiri likufuka utsi. Anthuwo atamva komanso kuona zimenezi ananjenjemera ndipo anaima patali.+ 19 Choncho anthuwo anauza Mose kuti: “Iweyo uzilankhula ndi ife, ndipo ife tizimvetsera, koma Mulungu asalankhule ndi ife kuopera kuti tingafe.”+
-