12 Chenjerani abale kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo nʼkukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+ 13 Mʼmalomwake, pitirizani kulimbikitsana tsiku ndi tsiku, nthawi iliyonse imene mukuti “Lero,”+ kuti chinyengo champhamvu cha uchimo chisaumitse mtima wa aliyense wa inu.