-
Mateyu 5:34-37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Koma ine ndikukuuzani kuti: Musamalumbire nʼkomwe,+ kutchula kumwamba, chifukwa nʼkumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu, 35 kapena kutchula dziko lapansi chifukwa ndi chopondapo mapazi ake,+ kapenanso kutchula Yerusalemu chifukwa ndi mzinda wa Mfumu yamphamvu.+ 36 Musamalumbire potchula mutu wanu, chifukwa simungathe kusandutsa tsitsi lanu, ngakhale limodzi, kuti likhale loyera kapena lakuda. 37 Tangotsimikizani kuti mukati ‘Indeʼ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayiʼ akhaledi ayi,+ chifukwa mawu owonjezera pamenepa ndi ochokera kwa woipayo.+
-