-
Aroma 13:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Chifukwa olamulira amaopsa ngati ukuchita zoipa, osati ngati ukuchita zabwino.+ Choncho kodi ukufuna kuti usamaope olamulira? Pitiriza kuchita zabwino,+ ndipo olamulira adzakutamanda. 4 Olamulirawo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zikuyendere bwino. Koma ngati ukuchita zoipa, chita mantha chifukwa sagwira lupanga pachabe, popeza iwo ndi mtumiki wa Mulungu wosonyeza mkwiyo wa Mulungu kwa munthu wochita zoipa.
-