-
Chivumbulutso 19:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Zimenezi zitatha, ndinamva mawu kumwamba amene ankamveka ngati mawu ofuula a khamu lalikulu akuti: “Tamandani Ya!*+ Mulungu wathu amapulumutsa anthu ndipo ali ndi mphamvu zazikulu komanso ulemerero, 2 chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi chiwerewere* chake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”*+
-