40 Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza,+ nthambi za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi yamʼchigwa.* Mukatero muzisangalala+ kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+
13 Choncho anatenga nthambi za kanjedza nʼkutuluka kukamuchingamira. Ndipo anayamba kufuula kuti: “Mʼpulumutseni! Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova,*+ amene ndi Mfumu ya Isiraeli!”+