19 Nyumba yopatulika yapakachisi wa Mulungu kumwamba inatsegulidwa ndipo likasa la pangano lake linaonekera lili mʼnyumba yake yopatulika yapakachisi.+ Ndiyeno kunachitika mphezi, kunamveka mawu, kunagunda mabingu, kunachita chivomerezi ndipo kunagwa matalala ambiri.