Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
140 Inu Yehova, ndipulumutseni kwa anthu oipa.
Nditetezeni kwa anthu ochita zachiwawa,+
2 Anthu amene amakonza chiwembu mʼmitima yawo+
Ndipo amayambitsa mikangano tsiku lonse.
4 Inu Yehova, nditetezeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+
Nditetezeni kwa anthu amene amachita zachiwawa.
Amene amakonza chiwembu kuti andivulaze.
5 Anthu onyada anditchera msampha.
Iwo agwiritsa ntchito zingwe kuti atchere ukonde mʼmphepete mwa njira,+
Ndipo anditchera makhwekhwe.+ (Selah)
6 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.
Mvetserani inu Yehova, kuchonderera kwanga kopempha thandizo.”+
7 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, Mpulumutsi wanga wamphamvu,
Mwateteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+
8 Inu Yehova, musapatse anthu oipa zimene amalakalaka.
Musalole kuti ziwembu zawo zitheke kuti angayambe kunyada.+ (Selah)
10 Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+
11 Munthu wonenera anzake zoipa asapeze malo padziko lapansi.*+
Zoipa zisakesake anthu ochita zachiwawa ndipo ziwawononge.