Salimo
Nyimbo yoimba polira imene Davide anaimbira Yehova, yokhudza mawu a Kusi wa fuko la Benjamini.
7 Inu Yehova Mulungu wanga, ine ndathawira kwa inu.+
Ndipulumutseni kwa anthu onse amene akundizunza ndipo mundilanditse.+
2 Mukapanda kutero andikhadzulakhadzula ngati mmene mkango umachitira,+
Nʼkunditenga popanda wondipulumutsa.
3 Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndalakwitsa chilichonse,
Ngati ndachita zinthu mopanda chilungamo,
4 Ngati ndachita zoipa kwa munthu amene akundichitira zabwino,+
Kapena ngati mdani wanga ndamulanda zinthu zake popanda chifukwa,*
5 Mdani wanga andithamangitse nʼkundipeza,
Andigwetsere pansi nʼkundipondaponda mpaka kufa
Ndipo andisiye nditagona pafumbi mwamanyazi. (Selah)
6 Nyamukani mutakwiya, inu Yehova.
Imirirani ndi kukhaulitsa adani anga amene andikwiyira.+
Dzukani nʼkundithandiza, ndipo mulamule kuti chilungamo chichitike.+
7 Mitundu ya anthu ikuzungulireni,
Ndipo inu muwaweruze muli kumwambako.
8 Yehova adzapereka chigamulo kwa mitundu ya anthu.+
Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changa
Komanso mogwirizana ndi kukhulupirika kwanga.+
9 Chonde, thetsani zinthu zoipa zimene anthu oipa akuchita.
Koma muchititse kuti wolungama akhale wolimba,+
Chifukwa inu ndinu Mulungu wolungama+ amene amayeza mitima+ komanso mmene munthu akumvera mumtima.*+
10 Mulungu ndi chishango changa,+ Mpulumutsi wa anthu owongoka mtima.+
13 Iye amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito zida zake zoopsa,
Amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito mivi yake yoyaka moto.+
14 Taonani munthu amene ali ndi pakati pa zinthu zoipa,
Watenga pakati pa mavuto ndipo adzabereka mabodza.+