Zekariya
10 “Pemphani Yehova kuti akugwetsereni mvula pa nthawi ya mvula yomalizira.
Yehova ndi amene amapanga mitambo yamvula,
Ndiponso amene amagwetsera anthu mvula.+
Iye amakulitsa mbewu mʼmunda mwa munthu aliyense.
Amafotokoza maloto opanda pake,
Ndipo saphula kanthu polimbikitsa anthu.
Nʼchifukwa chake adzasochere ngati nkhosa.
Iwo adzavutika chifukwa adzakhala opanda mʼbusa.
3 Ine ndakwiyira kwambiri abusa,
Ndipo atsogoleri awo opondereza* ndiwaimba mlandu.
Chifukwa ine Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndacheukira gulu langa la nkhosa+ lomwe ndi nyumba ya Yuda
Ndipo ndalisandutsa hatchi yanga yaulemerero, yokwera popita kunkhondo.
4 Mʼnyumba ya Yuda mudzatuluka mtsogoleri.
Mudzatulukanso wolamulira wothandiza,
Komanso mudzatuluka uta womenyera nkhondo.
Woyangʼanira* aliyense adzatuluka mwa iye. Onse adzatulukira limodzi.
5 Onsewa adzakhala ngati asilikali.
Adzapondaponda matope a mʼmisewu ya kunkhondo.
Ndidzawabwezera pamalo awo amene ankakhala,
Chifukwa ndidzawachitira chifundo.+
Iwo adzakhala ngati sanakanidwepo chiyambire.+
Popeza ine ndine Yehova Mulungu wawo, ndidzawayankha.
7 A nyumba ya Efuraimu adzakhala ngati msilikali wamphamvu,
Ndipo mumtima mwawo adzasangalala ngati amwa vinyo.+
Ana awo aamuna adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.
Mitima yawo idzakondwera chifukwa cha Yehova.+
8 ‘Ndidzawaitana ndi likhweru nʼkuwasonkhanitsa pamodzi.
Popeza ndidzawawombola,+ iwo adzachuluka.
Ndipo adzapitiriza kuchuluka.
9 Ngakhale kuti ndidzawamwaza ngati mbewu pakati pa anthu a mitundu ina,
Iwo adzandikumbukira ali kumadera akutali.
Iwowo ndi ana awo adzapezanso mphamvu ndipo adzabwerera.
10 Ndidzawabweretsa kuchokera kudziko la Iguputo.
Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kudziko la Asuri.+
Ndidzawabweretsa kudera la Giliyadi+ ndi la Lebanoni
Ndipo malo okwanira anthu onsewo sadzapezeka.+
11 Ndidzadutsa panyanja, nyanjayo nditaigwetsera tsoka.
Ndidzamenya mafunde a nyanjayo,+
Ndipo madzi onse a mtsinje wa Nailo adzauma.
Kunyada kwa Asuri kudzathetsedwa,
Ndipo ndodo yachifumu ya Iguputo idzachoka.+