Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
47 Inu anthu nonse, ombani mʼmanja.
Fuulani mosangalala chifukwa Mulungu wapambana.
2 Chifukwa Yehova, Wamʼmwambamwamba ndi wochititsa mantha,+
Iye ndi Mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.+
3 Iye amagonjetsa mitundu ya anthu kuti tiziilamulira.
Amaika mitundu ya anthu pansi pa mapazi athu.+
5 Mulungu wakwera kumalo ake, anthu akufuula mosangalala,
Yehova wakwera kumalo ake, anthu akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.
6 Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda.
Imbani nyimbo zotamanda Mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.
7 Chifukwa Mulungu ndi Mfumu ya dziko lonse lapansi.+
Imbani nyimbo zotamanda ndiponso sonyezani kuti ndinu ozindikira.
8 Mulungu wakhala Mfumu ya mitundu ya anthu.+
Mulungu wakhala pampando wake wachifumu wopatulika.
9 Atsogoleri a mitundu ya anthu asonkhana pamodzi
Ndi anthu a Mulungu wa Abulahamu.
Chifukwa Mulungu ali ndi mphamvu pa olamulira a* dziko lapansi.
Iye ndi wokwezeka kwambiri.+