Salimo
114 Isiraeli atatuluka mu Iguputo,+
Nyumba ya Yakobo itatuluka pakati pa anthu olankhula chilankhulo chachilendo,
2 Yuda anakhala malo ake opatulika,
Ndipo Isiraeli linakhala dziko limene ankalilamulira.+
5 Nʼchiyani chinakupangitsa kuti uthawe, nyanja iwe?+
Nʼchifukwa chiyani iwe Yorodano unabwerera mʼmbuyo?+
6 Nanga inu mapiri, nʼchifukwa chiyani munkadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo?
Inunso zitunda, nʼchifukwa chiyani munkadumphadumpha ngati ana a nkhosa?