Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
123 Ndakweza maso anga kuyangʼana inu,+
Inu amene mpando wanu wachifumu uli kumwamba.
2 Mofanana ndi mmene maso a atumiki amayangʼanira dzanja la mbuye wawo,
Komanso mmene maso a kapolo wamkazi amayangʼanira dzanja la mbuye wake wamkazi,
Maso athu akuyangʼana kwa Yehova Mulungu wathu,+
Mpakana atatikomera mtima.+
3 Tikomereni mtima, inu Yehova, tikomereni mtima,
Chifukwa tanyozeka kwambiri.+
4 Anthu odzikuza atinyoza kwambiri
Ndipo anthu onyada atichitira zachipongwe.