Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe. Salimo la Davide.
61 Inu Mulungu, imvani kulira kwanga kopempha thandizo.
Mvetserani pemphero langa mwatcheru.+
2 Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi ndidzafuulira inu
Pamene mtima wanga walefuka.+
Nditsogolereni nʼkundikweza pathanthwe lalitali kuposa msinkhu wanga.+
3 Chifukwa inu ndinu malo anga othawirako,
Nsanja yolimba imene imanditeteza kwa mdani.+
4 Ndidzakhala mlendo mutenti yanu mpaka kalekale.+
Ndidzabisala mumthunzi wa mapiko anu.+ (Selah)
5 Chifukwa inu Mulungu, mwamva malonjezo anga.
Mwandipatsa cholowa chimene ndi cha anthu amene amaopa dzina lanu.+
6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu,+
Ndipo idzakhala ndi moyo ku mibadwomibadwo.
7 Mfumuyo idzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale pamaso pa Mulungu.+
Chikondi chanu chokhulupirika komanso kukhulupirika kwanu ziiteteze.+
8 Mukatero ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka kalekale,+
Pamene ndikukwaniritsa malonjezo anga tsiku ndi tsiku.+