Amosi
1 Awa ndi mawu a Amosi* amene anali mmodzi wa anthu oweta nkhosa ku Tekowa.+ Anauzidwa mawu amenewa mʼmasomphenya okhudza Isiraeli, mʼmasiku a Uziya+ mfumu ya Yuda ndi mʼmasiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi,+ mfumu ya Isiraeli, kutatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike.+ 2 Iye anati:
“Yehova adzabangula ku Ziyoni,
Ndipo adzafuula ku Yerusalemu.
Malo amene abusa amadyetserako ziweto adzalira,
Ndipo pansonga ya phiri la Karimeli padzauma.”+
3 “Yehova wanena kuti,
‘“Popeza Damasiko anandigalukira mobwerezabwereza,* sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anapuntha Giliyadi ndi zida zopunthira zachitsulo.+
5 Ndidzathyola mipiringidzo ya mageti a Damasiko.+
Ndidzapha anthu a ku Bikati-aveni,
Komanso wolamulira* ku Beti-edeni.
Ndipo anthu a ku Siriya adzapita ku ukapolo ku Kiri,”+ watero Yehova.’
6 Yehova wanena kuti,
‘“Chifukwa chakuti Gaza+ wandigalukira mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anatenga anthu onse ogwidwa ukapolo+ nʼkuwapereka ku Edomu.
8 Ndidzapha anthu a ku Asidodi,+
Komanso wolamulira* wa ku Asikeloni.+
Ndidzalanga Ekironi,+
Ndipo ndidzafafaniza Afilisiti otsala,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’
9 Yehova wanena kuti,
‘Popeza Turo anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo,
Ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pachibale.+
11 Yehova wanena kuti,
‘Chifukwa Edomu wandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga,+
Komanso anakana kusonyeza chifundo.
Anapitiriza kuwakhadzulakhadzula,
Ndipo anapitirizabe kuwakwiyira kwambiri.+
13 Yehova wanena kuti,
‘“Chifukwa chakuti Aamoni andigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzawasinthira chigamulo changa.
Chifukwa anatumbula akazi apakati a ku Giliyadi kuti akulitse malo awo okhala.+
14 Ndidzayatsa mpanda wa Raba,+
Ndipo motowo udzawotcheratu nsanja zake zolimba.
Padzakhala mfuu ya nkhondo pa tsiku la nkhondo.
Komanso mphepo yamkuntho pa tsiku la chimvula champhamvu.
15 Ndipo mfumu yawo limodzi ndi akalonga ake adzapita ku ukapolo,”+ watero Yehova.’”