Salimo
Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
87 Maziko a mzinda wa Mulungu ali mʼmapiri opatulika.+
3 Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ (Selah)
4 Ndidzaika Rahabi* ndi Babulo mʼgulu la amene+ akundidziwa.
Filisitiya, Turo ndi Kusi alinso mʼgulu la amene akundidziwa.
Ine ndidzati: “Amenewa anabadwira mʼZiyoni.”
5 Ponena za Ziyoni anthu adzati:
“Aliyense anabadwira mmenemo.”
Ndipo Wamʼmwambamwamba adzakhazikitsa mzinda umenewo ndi kuulimbitsa.
6 Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:
“Amenewa anabadwira mu Ziyoni.” (Selah)
7 Oimba+ komanso ovina magule amene amavina mozungulira+ adzanena kuti: