Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la Genesis GENESIS ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Kulengedwa kwa dziko lapansi ndi kumwamba (1, 2) Masiku 6 okonza dziko lapansi (3-31) Tsiku Loyamba: kuwala; masana ndi usiku (3-5) Tsiku Lachiwiri: mlengalenga (6-8) Tsiku Lachitatu: mtunda ndi zomera (9-13) Tsiku la 4: zounikira zakumwamba (14-19) Tsiku la 5: nsomba ndi mbalame (20-23) Tsiku la 6: nyama ndi anthu (24-31) 2 Mulungu anapuma pa tsiku la 7 (1-3) Yehova Mulungu anapanga kumwamba ndi dziko lapansi (4) Mwamuna ndi mkazi mʼmunda wa Edeni (5-25) Munthu anapangidwa kuchokera kudothi (7) Mtengo woletsedwa wodziwitsa chabwino ndi choipa (15-17) Kulengedwa kwa mkazi (18-25) 3 Kuchimwa kwa munthu (1-13) Bodza loyamba (4, 5) Chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa opanduka (14-24) Ananeneratu za mbadwa ya mkazi (15) Anathamangitsidwa mu Edeni (23, 24) 4 Kaini ndi Abele (1-16) Mbadwa za Kaini (17-24) Seti ndi mwana wake Enosi (25, 26) 5 Kuyambira pa Adamu kudzafika pa Nowa (1-32) Adamu anabereka ana aamuna ndi aakazi (4) Inoki anayenda ndi Mulungu (21-24) 6 Ana a Mulungu anakwatira akazi padziko lapansi (1-3) Kubadwa kwa Anefili (4) Yehova anamva chisoni chifukwa cha kuipa kwa anthu (5-8) Nowa anapatsidwa ntchito yopanga chingalawa (9-16) Mulungu ananena kuti adzabweretsa chigumula (17-22) 7 Kulowa mʼchingalawa (1-10) Chigumula cha dziko lonse (11-24) 8 Kuphwa kwa madzi a chigumula (1-14) Anatumiza njiwa (8-12) Kutuluka mʼchingalawa (15-19) Lonjezo la Mulungu lokhudza dziko lapansi (20-22) 9 Malangizo opita kwa anthu onse (1-7) Lamulo lokhudza magazi (4-6) Pangano la utawaleza (8-17) Maulosi okhudza mbadwa za Nowa (18-29) 10 Mitundu ya anthu (1-32) Mbadwa za Yafeti (2-5) Mbadwa za Hamu (6-20) Nimurodi anatsutsana ndi Yehova (8-12) Mbadwa za Semu (21-31) 11 Nsanja ya Babele (1-4) Yehova anasokoneza chilankhulo (5-9) Kuchokera pa Semu kudzafika pa Abulamu (10-32) Banja la Tera (27) Abulamu anachoka ku Uri (31) 12 Abulamu anachoka ku Harana kupita ku Kanani (1-9) Lonjezo la Mulungu kwa Abulamu (7) Abulamu ndi Sarai ku Iguputo (10-20) 13 Abulamu anabwerera ku Kanani (1-4) Abulamu anasiyana ndi Loti (5-13) Mulungu anabwereza lonjezo lake kwa Abulamu (14-18) 14 Abulamu anapulumutsa Loti (1-16) Melekizedeki anadalitsa Abulamu (17-24) 15 Pangano la Mulungu ndi Abulamu (1-21) Ananeneratu kuti adzazunzidwa kwa zaka 400 (13) Mulungu anabwereza lonjezo lake kwa Abulamu (18-21) 16 Hagara ndi Isimaeli (1-16) 17 Abulahamu adzakhala tate wa mitundu yambiri (1-8) Dzina la Abulamu linasinthidwa kukhala Abulahamu (5) Pangano la mdulidwe (9-14) Dzina la Sarai linasinthidwa kukhala Sara (15-17) Analonjezedwa za kubadwa kwa Isaki (18-27) 18 Angelo atatu anapita kwa Abulahamu (1-8) Analonjeza kuti Sara adzabereka mwana wamwamuna; Sara anaseka (9-15) Abulahamu anapempha zokhudza Sodomu (16-33) 19 Angelo anapita kwa Loti (1-11) Loti ndi banja lake anauzidwa kuti asamuke (12-22) Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora (23-29) Mkazi wa Loti anasanduka chipilala chamchere (26) Loti ndi ana ake aakazi (30-38) Kumene Amowabu ndi Aamoni anachokera (37, 38) 20 Sara anapulumutsidwa kwa Abimeleki (1-18) 21 Kubadwa kwa Isaki (1-7) Isimaeli ankaseka Isaki (8, 9) Hagara ndi Isimaeli anathamangitsidwa (10-21) Pangano la Abulahamu ndi Abimeleki (22-34) 22 Abulahamu anauzidwa kuti apereke Isaki nsembe (1-19) Madalitso chifukwa cha mbadwa ya Abulahamu (15-18) Banja la Rabeka (20-24) 23 Imfa ya Sara komanso manda ake (1-20) 24 Anafunira Isaki mkazi (1-58) Rabeka anapita kukakumana ndi Isaki (59-67) 25 Abulahamu anakwatiranso (1-6) Imfa ya Abulahamu (7-11) Ana a Isimaeli (12-18) Kubadwa kwa Yakobo ndi Esau (19-26) Esau anagulitsa ukulu wake (27-34) 26 Isaki ndi Rabeka ku Gerari (1-11) Mulungu anatsimikizira lonjezo lake kwa Isaki (3-5) Kukanganirana zitsime (12-25) Pangano la Isaki ndi Abimeleki (26-33) Akazi awiri a Chihiti a Esau (34, 35) 27 Yakobo anadalitsidwa ndi Isaki (1-29) Esau ankafuna madalitso koma sanalape (30-40) Esau anayamba kudana ndi Yakobo (41-46) 28 Isaki anatumiza Yakobo ku Padani-aramu (1-9) Maloto a Yakobo ku Beteli (10-22) Mulungu anatsimikizira Yakobo za lonjezo lake (13-15) 29 Yakobo anakumana ndi Rakele (1-14) Yakobo anakonda Rakele (15-20) Yakobo anakwatira Leya ndi Rakele (21-29) Ana 4 aamuna a Yakobo amene Leya anamuberekera: Rubeni, Simiyoni, Levi ndi Yuda (30-35) 30 Biliha anabereka Dani ndi Nafitali (1-8) Zilipa anabereka Gadi ndi Aseri (9-13) Leya anabereka Isakara ndi Zebuloni (14-21) Rakele anabereka Yosefe (22-24) Ziweto za Yakobo zinachuluka (25-43) 31 Yakobo anachoka ku Kanani mozemba (1-18) Labani anapezana ndi Yakobo (19-35) Pangano la Yakobo ndi Labani (36-55) 32 Angelo anakumana ndi Yakobo (1, 2) Yakobo anakonzekera kukumana ndi Esau (3-23) Yakobo analimbana ndi mngelo (24-32) Yakobo anasinthidwa dzina kukhala Isiraeli (28) 33 Yakobo anakumana ndi Esau (1-16) Yakobo anapita ku Sekemu (17-20) 34 Dina anagwiriridwa (1-12) Ana a Yakobo anachita zinthu mwachinyengo (13-31) 35 Yakobo anachotsa milungu yachilendo (1-4) Yakobo anabwerera ku Beteli (5-15) Kubadwa kwa Benjamini; imfa ya Rakele (16-20) Ana 12 a Isiraeli (21-26) Imfa ya Isaki (27-29) 36 Mbadwa za Esau (1-30) Mafumu a ku Edomu (31-43) 37 Maloto a Yosefe (1-11) Yosefe ndi abale ake ansanje (12-24) Yosefe anagulitsidwa ku ukapolo (25-36) 38 Yuda ndi Tamara (1-30) 39 Yosefe mʼnyumba ya Potifara (1-6) Yosefe anakana kugona ndi mkazi wa Potifara (7-20) Yosefe anaikidwa mʼndende (21-23) 40 Yosefe anamasulira maloto a akaidi (1-19) ‘Mulungu ndi amene amamasulira’ (8) Phwando lokondwerera tsiku lobadwa la Farao (20-23) 41 Yosefe anamasulira maloto a Farao (1-36) Yosefe anapatsidwa udindo ndi Farao (37-46a) Yosefe ankayangʼanira ntchito yogawa chakudya (46b-57) 42 Azichimwene ake a Yosefe anapita ku Iguputo (1-4) Yosefe anakumana ndi azichimwene ake ndipo anawayesa (5-25) Azichimwene ake a Yosefe anabwerera kwa Yakobo (26-38) 43 Ulendo wachiwiri wa azichimwene ake a Yosefe wopita ku Iguputo limodzi ndi Benjamini (1-14) Yosefe anakumananso ndi azichimwene ake (15-23) Phwando la Yosefe ndi azichimwene ake (24-34) 44 Kapu yasiliva ya Yosefe inapezeka mʼthumba la Benjamini (1-17) Yuda anapempha kuti akhale kapolo mʼmalo mwa Benjamini (18-34) 45 Yosefe anadziulula kwa azichimwene ake (1-15) Azichimwene ake a Yosefe anabwerera kwawo kukatenga Yakobo (16-28) 46 Yakobo ndi banja lake anasamukira ku Iguputo (1-7) Mayina a anthu amene anasamukira ku Iguputo (8-27) Yosefe anakumana ndi Yakobo ku Goseni (28-34) 47 Yakobo anakumana ndi Farao (1-12) Yosefe anagwira ntchito yoyangʼanira mwanzeru (13-26) Isiraeli anakhazikika ku Goseni (27-31) 48 Yakobo anadalitsa ana awiri a Yosefe (1-12) Efuraimu analandira madalitso ambiri (13-22) 49 Ulosi umene Yakobo ananena atatsala pangʼono kumwalira (1-28) Silo adzachokera mwa Yuda (10) Yakobo anapereka malangizo okhudza kuikidwa mʼmanda kwake (29-32) Imfa ya Yakobo (33) 50 Yosefe anaika mʼmanda Yakobo ku Kanani (1-14) Yosefe anatsimikizira abale ake kuti anawakhululukira (15-21) Masiku akumapeto kwa moyo wa Yosefe ndi imfa yake (22-26) Lamulo la Yosefe lokhudza mafupa ake (25)