Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la 1 Mafumu 1 MAFUMU ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Davide ndi Abisagi (1-4) Adoniya ankafuna kukhala mfumu (5-10) Zimene anachita Natani ndi Bati-seba (11-27) Davide analamula kuti Solomo adzozedwe kukhala mfumu (28-40) Adoniya anathawira kuguwa la nsembe (41-53) 2 Davide analangiza Solomo (1-9) Davide anamwalira; Solomo anakhala mfumu (10-12) Zimene Adoniya anachita zinamuphetsa (13-25) Abiyatara anathamangitsidwa; Yowabu anaphedwa (26-35) Simeyi anaphedwa (36-46) 3 Solomo anakwatira mwana wa Farao (1-3) Yehova anaonekera kwa Solomo mʼmaloto (4-15) Solomo anapempha nzeru (7-9) Solomo anaweruza azimayi awiri (16-28) 4 Ulamuliro wa Solomo (1-19) Zinthu zinkayenda bwino mu ulamuliro wa Solomo (20-28) Aliyense anali wotetezeka pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi wa mkuyu (25) Nzeru za Solomo ndi miyambi yake (29-34) 5 Mfumu Hiramu anapereka zipangizo zomangira (1-12) Antchito yokakamiza a Solomo (13-18) 6 Solomo anamanga kachisi (1-38) Chipinda chamkati (19-22) Akerubi (23-28) Zogoba, zitseko, bwalo lamkati (29-36) Anamanga kachisi zaka pafupifupi 7 (37, 38) 7 Nyumba yachifumu ya Solomo (1-12) Hiramu waluso anathandiza Solomo (13-47) Zipilala ziwiri zakopa (15-22) Thanki yosungira madzi (23-26) Zotengera 10 zakopa (27-39) Anamaliza kupanga zinthu zagolide (48-51) 8 Anabweretsa Likasa mʼkachisi (1-13) Solomo analankhula ndi anthu (14-21) Pemphero la Solomo lotsegulira kachisi (22-53) Solomo anadalitsa anthu (54-61) Nsembe ndi chikondwerero chotsegulira kachisi (62-66) 9 Yehova anaonekeranso kwa Solomo (1-9) Mphatso zimene Solomo anapatsa Hiramu (10-14) Zinthu zimene Solomo anamanga (15-28) 10 Mfumukazi ya ku Sheba inakaona Solomo (1-13) Chuma chambiri cha Solomo (14-29) 11 Akazi a Solomo anapotoza mtima wake (1-13) Anthu amene ankalimbana ndi Solomo (14-25) Yerobowamu analonjezedwa mafuko (26-40) Solomo anamwalira; Rehobowamu anakhala mfumu (41-43) 12 Rehobowamu sanayankhe bwino anthu (1-15) Mafuko 10 anagalukira Solomo (16-19) Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli (20) Rehobowamu anamuletsa kuti asakamenyane ndi Aisiraeli (21-24) Yerobowamu anayamba kulambira mwana wa ngʼombe (25-33) 13 Ulosi wonena za guwa la ku Beteli (1-10) Guwa linagumuka (5) Munthu wa Mulungu sanamvere (11-34) 14 Ulosi wa Ahiya wotsutsa Yerobowamu (1-20) Rehobowamu anayamba kulamulira ku Yuda (21-31) Sisaki anaukira Yerusalemu (25, 26) 15 Abiyamu, mfumu ya Yuda (1-8) Asa, mfumu ya Yuda (9-24) Nadabu, mfumu ya Isiraeli (25-32) Basa, mfumu ya Isiraeli (33, 34) 16 Yehova anaweruza Basa (1-7) Ela, mfumu ya Isiraeli (8-14) Zimiri, mfumu ya Isiraeli (15-20) Omuri, mfumu ya Isiraeli (21-28) Ahabu, mfumu ya Isiraeli (29-33) Hiyeli anamanganso Yeriko (34) 17 Mneneri Eliya analosera chilala (1) Akhwangwala ankabweretsera Eliya chakudya (2-7) Eliya anapita kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati (8-16) Mwana wa mkazi wamasiye anamwalira nʼkuukitsidwa (17-24) 18 Eliya anakumana ndi Obadiya ndi Ahabu (1-18) Eliya ndi aneneri a Baala paphiri la Karimeli (19-40) ‘Mukayikakayika mpaka liti?’ (21) Chilala cha zaka zitatu ndi hafu chinatha (41-46) 19 Eliya anathawa Yezebeli (1-8) Yehova anaonekera kwa Eliya ku Horebe (9-14) Eliya anadzoza Hazaeli, Yehu ndi Elisa (15-18) Elisa anadzozedwa kuti alowe mʼmalo mwa Eliya (19-21) 20 Asiriya anamenyana ndi Ahabu (1-12) Ahabu anagonjetsa Asiriya (13-34) Ulosi wotsutsana ndi Ahabu (35-43) 21 Ahabu anasirira munda wa Naboti (1-4) Yezebeli anakonza zoti Naboti aphedwe (5-16) Uthenga wa Eliya wotsutsa Ahabu (17-26) Ahabu anadzichepetsa (27-29) 22 Yehosafati anachita mgwirizano ndi Ahabu (1-12) Mikaya analosera kuti Ahabu agonjetsedwa (13-28) Mzimu wabodza unapusitsa Ahabu (21, 22) Ahabu anaphedwa ku Ramoti-giliyadi (29-40) Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda (41-50) Ahaziya mfumu ya Isiraeli (51-53)