Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la 2 Mafumu 2 MAFUMU ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Eliya analosera za imfa ya Ahaziya (1-18) 2 Eliya anatengedwa ndi mphepo yamkuntho (1-18) Elisa anatenga chovala chauneneri cha Eliya (13, 14) Elisa anachititsa kuti madzi a ku Yeriko akhale abwino (19-22) Zimbalangondo zinapha anyamata a ku Beteli (23-25) 3 Yehoramu, mfumu ya Isiraeli (1-3) Amowabu anagalukira Isiraeli (4-25) Amowabu anagonjetsedwa (26, 27) 4 Elisa anachulukitsa mafuta a mkazi wamasiye (1-7) Mtima wochereza wa mayi wa ku Sunemu (8-16) Mayi anakhala ndi mwana; mwanayo anamwalira (17-31) Elisa anaukitsa mwana (32-37) Elisa anachotsa poizoni mʼchakudya (38-41) Elisa anachulukitsa mikate (42-44) 5 Elisa anachiritsa khate la Namani (1-19) Gehazi wadyera anakhala wakhate (20-27) 6 Elisa anayandamitsa nkhwangwa (1-7) Elisa ndi Asiriya (8-23) Maso a mtumiki wa Elisa anatsegulidwa (16, 17) Asiriya anachititsidwa khungu lamaganizo (18, 19) Mumzinda wa Samariya munali njala chifukwa choti unazunguliridwa (24-33) 7 Elisa analosera za kutha kwa njala (1, 2) Chakudya chinangosiyidwa mumsasa wa Asiriya (3-15) Ulosi wa Elisa unakwaniritsidwa (16-20) 8 Mayi wa ku Sunemu anabwezeredwa malo ake (1-6) Elisa, Beni-hadadi ndi Hazaeli (7-15) Yehoramu, mfumu ya Yuda (16-24) Ahaziya, mfumu ya Yuda (25-29) 9 Yehu anadzozedwa kukhala mfumu ya Isiraeli (1-13) Yehu anapha Yehoramu ndi Ahaziya (14-29) Yezebeli anaphedwa; agalu anadya thupi lake (30-37) 10 Yehu anapha anthu amʼbanja la Ahabu (1-17) Yehonadabu anagwirizana ndi Yehu (15-17) Yehu anapha anthu olambira Baala (18-27) Ulamuliro wa Yehu (28-36) 11 Ataliya analanda ufumu (1-3) Yehoasi anavekedwa ufumu mobisa (4-12) Ataliya anaphedwa (13-16) Yehoyada anasintha zinthu (17-21) 12 Yehoasi mfumu ya Yuda (1-3) Yehoasi anakonza kachisi (4-16) Asiriya anaukira (17, 18) Yehoasi anaphedwa (19-21) 13 Yehoahazi mfumu ya Isiraeli (1-9) Yehoasi mfumu ya Isiraeli (10-13) Elisa anayesa khama la Yehoasi (14-19) Elisa anamwalira; mafupa ake anaukitsa munthu (20, 21) Ulosi womaliza wa Elisa unakwaniritsidwa (22-25) 14 Amaziya, mfumu ya Yuda (1-6) Amaziya anamenyana ndi Aedomu ndi Aisiraeli (7-14) Imfa ya Yehoasi wa ku Isiraeli (15, 16) Imfa ya Amaziya (17-22) Yerobowamu Wachiwiri, mfumu ya Isiraeli (23-29) 15 Azariya, mfumu ya Yuda (1-7) Mafumu omaliza a Yuda: Zekariya (8-12), Salumu (13-16), Menahemu (17-22), Pekahiya (23-26), Peka (27-31) Yotamu, mfumu ya Yuda (32-38) 16 Ahazi, mfumu ya Yuda (1-6) Ahazi anapereka ziphuphu kwa Asuri (7-9) Ahazi anatengera mapulani a guwa la mulungu wonama (10-18) Imfa ya Ahazi (19, 20) 17 Hoshiya, mfumu ya Isiraeli (1-4) Kugonjetsedwa kwa Isiraeli (5, 6) Aisiraeli anapita ku ukapolo chifukwa cha mpatuko (7-23) Anthu a mitundu ina anabweretsedwa mʼmizinda ya ku Samariya (24-26) Ku Samariya kunali zipembedzo zosiyanasiyana (27-41) 18 Hezekiya, mfumu ya Yuda (1-8) Kugonjetsedwa kwa ufumu wa Isiraeli (9-12) Senakeribu anaukira Yuda (13-18) Rabisake ananyoza Yehova (19-37) 19 Hezekiya anapempha thandizo kwa Yehova kudzera mwa Yesaya (1-7) Senakeribu anaopseza Yerusalemu (8-13) Pemphero la Hezekiya (14-19) Yesaya anafotokoza zimene Mulungu anayankha (20-34) Mngelo anapha Asuri 185,000 (35-37) 20 Hezekiya anadwala nʼkuchira (1-11) Anthu anatumidwa kuchokera ku Babulo (12-19) Imfa ya Hezekiya (20, 21) 21 Manase, mfumu ya Yuda; anapha anthu (1-18) Yerusalemu adzawonongedwa (12-15) Amoni, mfumu ya Yuda (19-26) 22 Yosiya, mfumu ya Yuda (1, 2) Malangizo okhudza kukonza kachisi (3-7) Anapeza buku la Chilamulo (8-13) Hulida analosera tsoka (14-20) 23 Yosiya anasintha zinthu (1-20) Anachita chikondwerero cha Pasika (21-23) Zinthu zinanso zimene Yosiya anasintha (24-27) Imfa ya Yosiya (28-30) Yehoahazi, mfumu ya Yuda (31-33) Yehoyakimu, mfumu ya Yuda (34-37) 24 Kugalukira kwa Yehoyakimu komanso imfa yake (1-7) Yehoyakini, mfumu ya Yuda (8, 9) Ayuda oyamba kupita ku Babulo (10-17) Zedekiya, mfumu ya Yuda; anagalukira (18-20) 25 Nebukadinezara anazungulira Yerusalemu (1-7) Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa; Ayuda enanso anapita ku Babulo (8-21) Gedaliya anaikidwa kuti azilamulira (22-24) Gedaliya anaphedwa; anthu anathawira ku Iguputo (25, 26) Yehoyakini anamasulidwa ku Babulo (27-30)