Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la 1 Mbiri 1 MBIRI ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Kuchokera pa Adamu kufika pa Abulahamu (1-27) Mbadwa za Abulahamu (28-37) Aedomu ndi mafumu awo (38-54) 2 Ana 12 a Isiraeli (1, 2) Mbadwa za Yuda (3-55) 3 Mbadwa za Davide (1-9) Mzere wa mafumu a mʼbanja la Davide (10-24) 4 Mbadwa zina za Yuda (1-23) Yabezi ndiponso pemphero lake (9, 10) Mbadwa za Simiyoni (24-43) 5 Mbadwa za Rubeni (1-10) Mbadwa za Gadi (11-17) Mbadwa za Hagara zinagonjetsedwa (18-22) Hafu ya fuko la Manase (23-26) 6 Mbadwa za Levi (1-30) Oimba pakachisi (31-47) Mbadwa za Aroni (48-53) Kumene Alevi ankakhala (54-81) 7 Mbadwa za Isakara (1-5), za Benjamini (6-12), za Nafitali (13), za Manase (14-19), za Efuraimu (20-29), ndi za Aseri (30-40) 8 Mbadwa za Benjamini (1-40) Anthu a mʼbanja la Sauli (33-40) 9 Mndandanda wa makolo atabwera kuchokera ku ukapolo (1-34) Kubwereza anthu a mʼbanja la Sauli (35-44) 10 Imfa ya Sauli ndi ana ake (1-14) 11 Aisiraeli onse anadzoza Davide kukhala mfumu (1-3) Davide analanda mzinda wa Ziyoni (4-9) Asilikali amphamvu a Davide (10-47) 12 Anthu amene anali kumbali ya ufumu wa Davide (1-40) 13 Likasa linatengedwa ku Kiriyati-yearimu (1-14) Uza anaphedwa (9, 10) 14 Ufumu wa Davide unakhazikika (1, 2) Banja la Davide (3-7) Afilisiti anagonjetsedwa (8-17) 15 Alevi anatenga Likasa kupita nalo ku Yerusalemu (1-29) Mikala ananyoza Davide (29) 16 Likasa linaikidwa mutenti (1-6) Nyimbo ya Davide yothokoza (7-36) “Yehova wakhala Mfumu!” (31) Utumiki wa kumene kunali Likasa (37-43) 17 Davide anauzidwa kuti sadzamanga kachisi (1-6) Pangano la ufumu ndi Davide (7-15) Pemphero la Davide loyamika (16-27) 18 Davide anapambana nkhondo zosiyanasiyana (1-13) Ulamuliro wa Davide (14-17) 19 Chipongwe chimene Aamoni anachitira atumiki a Davide (1-5) Aamoni ndi Asiriya anagonjetsedwa (6-19) 20 Raba anagonjetsedwa (1-3) Ziphona za Afilisiti zinaphedwa (4-8) 21 Davide anawerenga anthu mosavomerezeka (1-6) Chilango chochokera kwa Yehova (7-17) Davide anamanga guwa (18-30) 22 Davide anakonzekera zinthu zomangira kachisi (1-5) Davide anapereka malangizo kwa Solomo (6-16) Akalonga analamulidwa kuti athandize Solomo (17-19) 23 Davide anapereka ntchito kwa Alevi (1-32) Aroni ndi ana ake anasankhidwa kuti azigwira ntchito yopatulika (13) 24 Davide anagawa ansembe mʼmagulu 24 (1-19) Ntchito zina za Alevi (20-31) 25 Oimba panyumba ya Mulungu (1-31) 26 Magulu a alonda apageti (1-19) Oyangʼanira chuma ndi anthu a maudindo ena (20-32) 27 Anthu otumikira mfumu (1-34) 28 Zimene Davide ananena zokhudza kumanga kachisi (1-8) Solomo anapatsidwa malangizo komanso mapulani omangira (9-21) 29 Zopereka zothandiza pomanga kachisi (1-9) Pemphero la Davide (10-19) Anthu anasangalala; ufumu wa Solomo (20-25) Imfa ya Davide (26-30)