Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la 2 Mbiri 2 MBIRI ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Solomo anapempha nzeru (1-12) Chuma cha Solomo (13-17) 2 Kukonzekera kumanga kachisi (1-18) 3 Solomo anayamba kumanga kachisi (1-7) Malo Oyera Koposa (8-14) Zipilala ziwiri zakopa (15-17) 4 Guwa lansembe, thanki yosungira madzi ndi mabeseni (1-6) Zoikapo nyale, matebulo ndi mabwalo (7-11a) Kumaliza ntchito yomanga kachisi (11b-22) 5 Kukonzekera kutsegulira kachisi (1-14) Kubweretsa likasa kukachisi (2-10) 6 Solomo analankhula ndi anthu (1-11) Pemphero la Solomo lotsegulira kachisi (12-42) 7 Kachisi anadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova (1-3) Zikondwerero zotsegulira kachisi (4-10) Yehova anaonekera kwa Solomo (11-22) 8 Zinthu zina zimene Solomo anamanga (1-11) Anakonza dongosolo lolambirira pakachisi (12-16) Zombo za Solomo (17, 18) 9 Mfumukazi ya ku Sheba inapita kwa Solomo (1-12) Chuma cha Solomo (13-28) Imfa ya Solomo (29-31) 10 Aisiraeli anagalukira Rehobowamu (1-19) 11 Ulamuliro wa Rehobowamu (1-12) Alevi okhulupirika anasamukira ku Yuda (13-17) Banja la Rehobowamu (18-23) 12 Sisaki anaukira Yerusalemu (1-12) Kutha kwa ulamuliro wa Rehobowamu (13-16) 13 Abiya, mfumu ya Yuda (1-22) Abiya anagonjetsa Yerobowamu (3-20) 14 Imfa ya Abiya (1) Asa, mfumu ya Yuda (2-8) Asa anagonjetsa Aitiyopiya 1 miliyoni (9-15) 15 Zinthu zimene Asa anasintha (1-19) 16 Mgwirizano wa Asa ndi Siriya (1-6) Haneni anadzudzula Asa (7-10) Imfa ya Asa (11-14) 17 Yehosafati, mfumu ya Yuda (1-6) Ntchito yophunzitsa anthu (7-9) Asilikali amphamvu a Yehosafati (10-19) 18 Mgwirizano wa Yehosafati ndi Ahabu (1-11) Mikaya analosera zoti agonjetsedwa (12-27) Ahabu anaphedwa ku Ramoti-giliyadi (28-34) 19 Yehu anadzudzula Yehosafati (1-3) Zinthu zimene Yehosafati anasintha (4-11) 20 Mayiko ozungulira anayamba kuopseza Ayuda (1-4) Yehosafati anapempha Mulungu kuti amuthandize (5-13) Mmene Yehova anamuyankhira (14-19) Ayuda anapulumutsidwa modabwitsa (20-30) Kutha kwa ulamuliro wa Yehosafati (31-37) 21 Yehoramu, mfumu ya Yuda (1-11) Uthenga umene Eliya analemba (12-15) Mapeto omvetsa chisoni a Yehoramu (16-20) 22 Ahaziya, mfumu ya Yuda (1-9) Ataliya analanda ufumu (10-12) 23 Yehoyada anathandiza kuti Yehoasi akhale mfumu (1-11) Ataliya anaphedwa (12-15) Zinthu zomwe Yehoyada anasintha (16-21) 24 Ulamuliro wa Yehoasi (1-3) Yehoasi anakonza kachisi (4-14) Yehoasi anayamba kulambira mafano (15-22) Yehoasi anaphedwa (23-27) 25 Amaziya, mfumu ya Yuda (1-4) Anamenyana ndi Aedomu (5-13) Amaziya anayamba kulambira mafano (14-16) Anamenyana ndi Yehoasi mfumu ya Isiraeli (17-24) Imfa ya Amaziya (25-28) 26 Uziya, mfumu ya Yuda (1-5) Nkhondo zimene Uziya anamenya (6-15) Uziya anachititsidwa khate chifukwa chodzikuza (16-21) Imfa ya Uziya (22, 23) 27 Yotamu, mfumu ya Yuda (1-9) 28 Ahazi, mfumu ya Yuda (1-4) Anagonjetsedwa ndi Siriya komanso Isiraeli (5-8) Odedi anachenjeza Isiraeli (9-15) Ayuda anatsitsidwa (16-19) Ahazi anayamba kulambira mafano; imfa ya Ahazi (20-27) 29 Hezekiya, mfumu ya Yuda (1, 2) Zinthu zimene Hezekiya anasintha (3-11) Kuyeretsa kachisi (12-19) Anayambiranso utumiki wapakachisi (20-36) 30 Hezekiya anachita Pasika (1-27) 31 Hezekiya anathetsa kulambira mafano (1) Ansembe ndi Alevi anayamba kuthandizidwa (2-21) 32 Senakeribu anaopseza Yerusalemu (1-8) Senakeribu ananyoza Yehova (9-19) Mngelo anapha asilikali a Asiriya (20-23) Hezekiya anadwala kenako anadzikuza (24-26) Zimene Hezekiya anachita; imfa ya Hezekiya (27-33) 33 Manase, mfumu ya Yuda (1-9) Manase analapa machimo ake (10-17) Imfa ya Manase (18-20) Amoni, mfumu ya Yuda (21-25) 34 Yosiya, mfumu ya Yuda (1, 2) Zinthu zomwe Yosiya anasintha (3-13) Anapeza buku la Chilamulo (14-21) Hulida analosera za tsoka (22-28) Yosiya anawerengera anthu buku (29-33) 35 Yosiya anakonza zoti achite pasika (1-19) Yosiya anaphedwa ndi Farao Neko (20-27) 36 Yehoahazi, mfumu ya Yuda (1-3) Yehoyakimu, mfumu ya Yuda (4-8) Yehoyakini, mfumu ya Yuda (9, 10) Zedekiya, mfumu ya Yuda (11-14) Yerusalemu anawonongedwa (15-21) Koresi analamula kuti kachisi amangidwenso (22, 23)