Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili M‘buku la Hoseya HOSEYA ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Mkazi wa Hoseya ndiponso ana amene anabereka (1-9) Yezereeli (4), Lo-ruhama (6), ndi Lo-ami (9) Chiyembekezo cha kubwezeretsa komanso mgwirizano (10, 11) 2 Aisiraeli osakhulupirika analangidwa (1-13) Yehova anakhalanso mwamuna wawo (14-23) “Adzanditchula kuti Mwamuna wanga” (16) 3 Hoseya anagula mkazi wake wachigololo (1-3) Aisiraeli adzabwerera kwa Yehova (4, 5) 4 Yehova anali ndi mlandu woti aimbe Aisiraeli (1-8) Panalibe amene ankadziwa Mulungu mʼdzikolo (1) Aisiraeli ankalambira mafano komanso kuchita chiwerewere (9-19) Mtima wachiwerewere unawasocheretsa (12) 5 Chiweruzo cha Efuraimu ndi Yuda (1-15) 6 Anawauza kuti abwerere kwa Yehova (1-3) Anthu anasonyeza chikondi chokhulupirika chosakhalitsa (4-6) Chikondi chokhulupirika chimaposa nsembe (6) Anthu anali ndi khalidwe lochititsa manyazi (7-11) 7 Zoipa za Efuraimu (1-16) Sangathawe ukonde wa Mulungu (12) 8 Zotsatira za kulambira mafano (1-14) Kufesa mphepo, kukolola mphepo yamkuntho (7) Aisiraeli anaiwala amene anawapanga (14) 9 Mulungu anakana Efuraimu chifukwa cha machimo ake (1-17) Anadzipereka kwa mulungu wochititsa manyazi (10) 10 Aisiraeli, omwe ndi mtengo wa mpesa wowonongeka, adzawonongedwa (1-15) Kufesa ndiponso kukolola (12, 13) 11 Mulungu anakonda Isiraeli kuyambira ali mnyamata (1-12) ‘Ndinaitana mwana wanga kuti atuluke mu Iguputo’ (1) 12 Efuraimu ayenera kubwerera kwa Yehova (1-14) Yakobo analimbana ndi Mulungu (3) Yakobo analira kuti apeze madalitso a Mulungu (4) 13 Efuraimu anaiwala Yehova chifukwa cholambira mafano (1-16) ‘Imfa, kodi mphamvu yako ili kuti?’ (14) 14 Anapemphedwa kuti abwerere kwa Yehova (1-3) Kutamanda Mulungu ndi pakamwa (2) Aisiraeli osakhulupirika anachiritsidwa (4-9)