Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili M‘buku la Amosi AMOSI ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Amosi analandira uthenga wochokera kwa Yehova (1, 2) Ziweruzo chifukwa chogalukira mobwerezabwereza (3-15) Siriya (3-5), Filisitiya (6-8), Turo (9, 10), Edomu (11, 12), Amoni (13-15) 2 Ziweruzo chifukwa chogalukira mobwerezabwereza (1-16) Mowabu (1-3), Yuda (4, 5), Isiraeli (6-16) 3 Kulengeza uthenga wachiweruzo wa Mulungu (1-8) Mulungu anaulula chinsinsi chake (7) Uthenga wotsutsana ndi Samariya (9-15) 4 Uthenga wotsutsana ndi ngʼombe za ku Basana (1-3) Yehova ananyoza kulambira kwabodza kwa Aisiraeli (4, 5) Aisiraeli anakana kubwerera kwa Mulungu (6-13) “Konzekera kukumana ndi Mulungu wako” (12) ‘Mulungu amafotokozera munthu zimene akuganiza’ (13) 5 Isiraeli anali ngati namwali wakugwa (1-3) Funafunani Mulungu kuti mukhale ndi moyo (4-17) Muzidana ndi zoipa nʼkumakonda zabwino (15) Tsiku la Yehova ndi tsiku lamdima (18-27) Nsembe za Aisiraeli zinakanidwa (22) 6 Tsoka kwa anthu okhala mosatekeseka (1-14) Mabedi aminyanga ya njovu; makapu a vinyo (4, 6) 7 Masomphenya osonyeza kuti mapeto a Aisiraeli ali pafupi (1-9) Dzombe (1-3), moto (4-6), chingwe choyezera (7-9) Amosi anauzidwa kuti asiye kunenera (10-17) 8 Masomphenya a dengu la zipatso zamʼchilimwe (1-3) Anthu opondereza anzawo anadzudzulidwa (4-14) Njala yauzimu (11) 9 Nʼzosatheka kuthawa chiweruzo cha Mulungu (1-10) Nyumba ya Davide inadzutsidwanso (11-15)