Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili M‘buku la Zekariya ZEKARIYA ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Kuuza anthu kuti abwerere kwa Yehova (1-6) ‘Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu’ (3) Masomphenya Oyamba: Okwera pamahatchi ataima pamitengo ya mchisu (7-17) “Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni” (17) Masomphenya Achiwiri: Nyanga 4 ndi amisiri 4 (18-21) 2 Masomphenya Achitatu: Munthu atanyamula chingwe choyezera (1-13) Kuyeza Yerusalemu (2) Yehova, “mpanda wamoto” (5) Kukhudza mwana wa diso la Mulungu (8) Mitundu yambiri ya anthu idzakhala kumbali ya Yehova (11) 3 Masomphenya a 4: Kusintha zovala za mkulu wa ansembe (1-10) Satana ankatsutsa Mkulu wa Ansembe Yoswa (1) “Ndibweretsa mtumiki wanga dzina lake Mphukira” (8) 4 Masomphenya a 5: Choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi (1-14) ‘Sipakufunika mphamvu, koma mzimu wanga’ (6) Asakunyozeni chifukwa munayamba ndi zinthu zochepa (10) 5 Masomphenya a 6: Mpukutu ukuuluka (1-4) Masomphenya a 7: Chiwiya chokwana muyezo wa efa (5-11) Munali mzimayi dzina lake Kuipa (8) Chiwiya anachitenga nʼkupita nacho ku Sinara (9-11) 6 Masomphenya a 8: Magaleta 4 (1-8) Mphukira idzakhala mfumu ndi wansembe (9-15) 7 Yehova anadzudzula anthu osala kudya mwachinyengo (1-14) “Kodi munkasaladi kudya chifukwa cha ine?” (5) ‘Muzisonyeza chilungamo, chikondi chokhulupirika ndi chifundo’ (9) 8 Yehova anapatsa Ziyoni mtendere ndi choonadi (1-23) Yerusalemu, “mzinda wa choonadi” (3) “Muziuzana zoona” (16) Kusiya kusala kudya nʼkuyamba kuchita chikondwerero (18, 19) ‘Tifunefune Yehova’ (21) Amuna 10 adzagwira mkanjo wa Myuda (23) 9 Mulungu adzaweruza anthu a mitundu ina (1-8) Kubwera kwa mfumu ya Ziyoni (9, 10) Mfumu yodzichepetsa inakwera bulu (9) Anthu a Yehova adzamasulidwa (11-17) 10 Pemphani mvula kwa Yehova osati kwa milungu yabodza (1, 2) Yehova akugwirizanitsa anthu ake (3-12) Mtsogoleri wochokera mʼbanja la Yuda (3, 4) 11 Zotsatira za kukana mʼbusa weniweni wa Mulungu (1-17) “Weta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa” (4) Ndodo ziwiri: Wosangalatsa komanso Mgwirizano (7) Malipiro a mʼbusa: Ndalama 30 zasiliva (12) Ndalama zinaponyedwa mosungira chuma (13) 12 Yehova anateteza Yuda ndi Yerusalemu (1-9) Yerusalemu, “mwala wolemera” (3) Kulirira munthu amene anabayidwa (10-14) 13 Kuchotsa mafano ndi aneneri abodza (1-6) Aneneri abodza adzachita manyazi (4-6) Mʼbusa adzaphedwa (7-9) Anthu otsala adzayengedwa (9) 14 Kulambira koona kudzapambana (1-21) Phiri la Maolivi lidzagawikana pakati (4) Yehova adzakhala mmodzi, dzina lake lidzakhala limodzi (9) Mliri wa anthu otsutsa Yerusalemu (12-15) Chikondwerero cha Misasa (16-19) Mphika uliwonse udzakhala woyera kwa Yehova (20, 21)