Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili M‘buku la Malaki MALAKI ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Yehova amakonda anthu ake (1-5) Ansembe ankapereka nsembe zosalongosoka (6-14) Dzina la Mulungu lidzakhala lalikulu pakati pa anthu a mitundu ina (11) 2 Ansembe ankalephera kulangiza anthu (1-9) Ansembe ankayenera kuphunzitsa anthu za Mulungu (7) Anthu ankathetsa mabanja pa zifukwa zosamveka (10-17) “‘Ndimadana ndi zoti anthu azithetsa mabanja,’ watero Yehova” (16) 3 Ambuye woona anabwera kudzayeretsa kachisi (1-5) Mthenga wa pangano (1) Anawalimbikitsa kuti abwerere kwa Yehova (6-12) Yehova sasintha (6) “Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu” (7) ‘Bweretsani chakhumi chonse ndipo Yehova adzakudalitsani’ (10) Anthu olungama ndiponso anthu oipa (13-18) Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pa Mulungu (16) Kusiyana pakati pa wolungama ndi woipa (18) 4 Eliya adzabwera tsiku la Yehova lisanafike (1-6) ‘Dzuwa la chilungamo lidzawala’ (2)