MATEYU
ZIMENE ZILI MʼBUKULI
-
ULALIKI WAPAPHIRI (1-48)
Yesu anayamba kuphunzitsa paphiri (1, 2)
Zinthu 9 zimene zimapangitsa anthu kuti azikhala osangalala (3-12)
Mchere komanso kuwala (13-16)
Yesu anakwaniritsa Chilamulo (17-20)
Malangizo okhudza mkwiyo (21-26), chigololo (27-30), kutha kwa ukwati (31, 32), malumbiro (33-37), kubwezera (38-42), kukonda adani athu (43-48)
-
Yesu ndi “Mbuye wa Sabata” (1-8)
Anachiritsa munthu wolumala dzanja (9-14)
Mtumiki amene Mulungu amamukonda (15-21)
Anatulutsa ziwanda pogwiritsa ntchito mzimu woyera (22-30)
Tchimo losakhululukidwa (31, 32)
Mtengo umadziwika ndi zipatso zake (33-37)
Chizindikiro cha Yona (38-42)
Mzimu wonyansa ukabwerera (43-45)
Amayi ake a Yesu komanso azichimwene ake (46-50)
-
MAFANIZO OKHUDZA UFUMU (1-52)
Wofesa mbewu (1-9)
Chifukwa chake Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo (10-17)
Tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu (18-23)
Tirigu ndi namsongole (24-30)
Kanjere kampiru komanso zofufumitsa (31-33)
Kugwiritsa ntchito mafanizo kunakwaniritsa ulosi (34, 35)
Tanthauzo la fanizo la tirigu ndi namsongole (36-43)
Chuma chobisika ndi ngale yamtengo wapatali (44-46)
Khoka (47-50)
Chuma chatsopano ndi chakale (51, 52)
Yesu anakanidwa mʼdera lakwawo (53-58)
-
CHIZINDIKIRO CHA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-51)
-
Ansembe anakonza chiwembu kuti aphe Yesu (1-5)
Yesu anathiridwa mafuta onunkhira (6-13)
Pasika womaliza komanso kuperekedwa (14-25)
Anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (26-30)
Ananeneratu kuti Petulo adzamukana (31-35)
Yesu anapemphera ku Getsemane (36-46)
Yesu anagwidwa (47-56)
Anazengedwa mlandu ndi Khoti Lalikulu la Ayuda (57-68)
Petulo anakana Yesu (69-75)