Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la 2 Akorinto 2 AKORINTO ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Mawu oyamba (1, 2) Mulungu amatitonthoza pa vuto lililonse (3-11) Paulo anasintha mapulani a ulendo wake (12-24) 2 Paulo ankafuna kuti Akhristu a ku Korinto asangalale (1-4) Wochimwa anakhululukidwa nʼkubwezeretsedwa (5-11) Paulo anapita ku Torowa ndiponso ku Makedoniya (12, 13) Utumiki, kuguba ponyadira kupambana (14-17) Sitichita malonda ndi mawu a Mulungu (17) 3 Makalata otichitira umboni (1-3) Atumiki a pangano latsopano (4-6) Ulemerero wa pangano latsopano ndi waukulu (7-18) 4 Kuwala kwa uthenga wabwino (1-6) Maganizo a osakhulupirira anachititsidwa khungu (4) Chuma mʼzonyamulira zadothi (7-18) 5 Kuvala nyumba ya kumwamba (1-10) Utumiki wogwirizanitsa anthu ndi Mulungu (11-21) Cholengedwa chatsopano (17) Akazembe mʼmalo mwa Khristu (20) 6 Osagwiritsa ntchito molakwa kukoma mtima kwa Mulungu (1, 2) Utumiki wa Paulo (3-13) Musamangidwe mʼgoli ndi osakhulupirira (14-18) 7 Tidziyeretse kuchotsa choipitsa chilichonse (1) Paulo anasangalala ndi Akorinto (2-4) Tito anabwera ndi lipoti labwino (5-7) Chisoni chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndiponso kulapa (8-16) 8 Zopereka za Akhristu a ku Yudeya (1-15) Tito anatumizidwa ku Korinto (16-24) 9 Analimbikitsidwa kukhala opatsa (1-15) Mulungu amakonda wopereka mosangalala (7) 10 Paulo anafotokoza zokhudza utumiki wake (1-18) Zida zankhondo yathu si zochokera mʼdziko (4, 5) 11 Paulo ndiponso atumwi apamwamba (1-15) Mavuto amene mtumwi Paulo anakumana nawo (16-33) 12 Masomphenya a Paulo (1-7a) “Minga mʼthupi” la Paulo (7b-10) Sankachepa poyerekezera ndi atumwi apamwamba (11-13) Paulo ankadera nkhawa Akorinto (14-21) 13 Malangizo komanso machenjezo omaliza (1-14) “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro” (5) Kusintha maganizo; kukhala ndi maganizo ogwirizana (11)