Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la Yakobo YAKOBO ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Moni (1) Kupirira kumachititsa kuti tikhale osangalala (2-15) Chikhulupiriro chimakhala cholimba tikamayesedwa (3) Tizipempha ndi chikhulupiriro (5-8) Chilakolako chimabweretsa uchimo ndi imfa (14, 15) Mphatso iliyonse yabwino imachokera kumwamba (16-18) Kumva ndi kuchita zimene mawu akunena (19-25) Munthu amene akudziyangʼanira pagalasi (23, 24) Kulambira koyera komanso kosadetsedwa (26, 27) 2 Kuchita zokondera ndi tchimo (1-13) Chikondi ndi lamulo lachifumu (8) Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa (14-26) Ziwanda zimakhulupirira ndipo zimanjenjemera (19) Abulahamu ankadziwika kuti ndi mnzake wa Yehova (23) 3 Kuweta lilime (1-12) Pasakhale aphunzitsi ambiri (1) Nzeru yochokera kumwamba (13-18) 4 Musachite ubwenzi ndi dziko (1-12) Tsutsani Mdyerekezi (7) Yandikirani Mulungu (8) Anawachenjeza kuti apewe kunyada (13-17) “Yehova akalola” (15) 5 Anachenjeza anthu achuma (1-6) Mulungu amadalitsa anthu amene amayembekezera moleza mtima (7-11) Mukati “ayi,” azikhaladi ayi (12) Pemphero lachikhulupiriro limagwira ntchito (13-18) Kuthandiza munthu wochimwa kuti abwerere (19, 20)